Ndakatulo

 NDAPHUNZIRA NAWO ANTHU A MAINA


Ndisilira inu ana a mma 2000

Anu maina kukoma powatchula

Nkamwamu kuchita kuzuna ngati keke

Mumanyadirana potchulana anuwake

Mumvekere, Asante, Praise, Trinity, Favour, Junior ndi ena otero

Ndikakhala ine nde ndaphunzira nawo anthu a maina


Ndikutitu ndayimba nawo sukulu ine anthu a maina

Ukawatchula mwana kulira

Kuwalingalira wekha kuzizimuka

Pena ngati ukulota maloto oopsa

Ena atanthauzo ena ayi ntaaa

Achina Kanere, Viwisi, Mleza, Zinthambo, Mbulayanga, Toga ndi Zinthonga mpakana pano tanthauzo lawo silidziwika

Nabola achina Tembani, Mkakeni, Penjani, Thula ndi Mavuto matanthauzo awo ngoziwika

Inetu ndaphunzira nawo anthu a maina


Nawo a Phunzitsi athu a Songolo

Atasongola pampando kusogolo

Kutichosa umbuli kutipasa tsogolo

Koma ndikalingalira za kalasi la pa sogolo

Ine kugwidwa tsebwe ndi maina azifukwa

Achina Walekeni, Walyenge, Nyamazawo, Wafiske, Khumbolawo

Naoso akulimbikira kuopa tingawapeze

Kalasi lambuyo mwathu naloso silinalekelere

Kukhalanawo anthu a mainawa

Achina Lyaniso, Mloyiso, Viyezgo, Masuzgo, Mafayo ndi Phangwayo

Atapanilira maphunziro kuti azatipeze

Mbambadi ine ndaphunzira nawo anthu a maina

Comments