Ndakatulo by Tobby Elefunt

 Chimkhala ku Gospel kunali Beef


Wina ndi uja Zaubusa Za Mlaka Atanyamulidwa pa stage ngati Maliro

Kuli kuledzela kuopa vinyo angamuthereso

Chemwali aja nawo ayamba kuzitaya 

Ati ali Busy kulongosola ma Signal ku Jamaica 

Akakhala achimwene Dasitani nde paja Ngo Pitapita

Kukachasu nde kwawo poti wam'mabotolo kudula

Chimkhala ku gospel kunali beef


Mwana wa Malemu Chisomo nde tinamtuluka  

Kuchokera pompaja ana mu tChinga pakhomo la Pipozi

Atasenza chokoleti ndi masiwiti mmayala

Nabola yemweyu Loyidi mwana wa Mountain 

Olo atamangisa wake oyera atakalamba

Ndikuti atataka-tataka mokwanila ma nurse odzuna

Komabe tinyimbo take timatisunthira chifupi ndi Yahweh 

Mwina nafe mkanjo mkukaugwira

Tikutitu timakunyadirani Uncle Loyidi

Chimkhala ku gospel kunali beef


Uyu odalira alamuyu nde sitinena

Ankadziwa ndithu kuti zizakhala better ija

Amazitanthauza iye mwini

Pano anayiphula ngakhale ali yakali yakali mmakhoti

Kuyesesa kufuta mbiri yokupha mwana Nkhata

Komabe a Kondakitale ija anapha

Chimkhala ku gospel kunali beef


Sibwenzi Wakise K nzake wa Wikise ali busy ndi dzuna yake ija

Kujambulisa ma video ngati akukonzekera kujambulisa kanema olaura

Anuwake ati nkumati agwetserana mchikondi

Anthu ati mmmm nanu za uchisi izi

Ena nkumati "nabola sufi" ija anazibayira yekha

Komabe china nchina afanawa sadaname

Suffix uja amatha

Onsewa akanawabifa ndi verse imodzi

Mu "am drowning" 

Chimkhala ku gospel kunali beef

Comments

Popular posts from this blog

Lets Emulate Mbanandi

Exodus

John Jill Writes