Ndakatulo
NDAPHUNZIRA NAWO ANTHU A MAINA Ndisilira inu ana a mma 2000 Anu maina kukoma powatchula Nkamwamu kuchita kuzuna ngati keke Mumanyadirana potchulana anuwake Mumvekere, Asante, Praise, Trinity, Favour, Junior ndi ena otero Ndikakhala ine nde ndaphunzira nawo anthu a maina Ndikutitu ndayimba nawo sukulu ine anthu a maina Ukawatchula mwana kulira Kuwalingalira wekha kuzizimuka Pena ngati ukulota maloto oopsa Ena atanthauzo ena ayi ntaaa Achina Kanere, Viwisi, Mleza, Zinthambo, Mbulayanga, Toga ndi Zinthonga mpakana pano tanthauzo lawo silidziwika Nabola achina Tembani, Mkakeni, Penjani, Thula ndi Mavuto matanthauzo awo ngoziwika Inetu ndaphunzira nawo anthu a maina Nawo a Phunzitsi athu a Songolo Atasongola pampando kusogolo Kutichosa umbuli kutipasa tsogolo Koma ndikalingalira za kalasi la pa sogolo Ine kugwidwa tsebwe ndi maina azifukwa Achina Walekeni, Walyenge, Nyamazawo, Wafiske, Khumbolawo Naoso akulimbikira kuopa tingawapeze Kalasi lambuyo mwathu naloso silinalekelere Kukhalana...